Ndipo munthu akabwera nacho chopereka ndicho nsembe yaufa ya kwa Yehova, chopereka chake chizikhala cha ufa wosalala; ndipo athirepo mafuta, ndi kuikapo lubani.
Numeri 29:18 - Buku Lopatulika ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira, za ng'ombe, za nkhosa zamphongo, ndi za anaankhosa, monga mwa kuwerenga kwake, ndi kutsata lemba lake; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira, za ng'ombe, za nkhosa zamphongo, ndi za anaankhosa, monga mwa kuwerenga kwake, ndi kutsata lemba lake; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa pamodzi ndi chopereka cha chakudya ndi cha chakumwa pa ng'ombe zamphongo zija, pa nkhosa zamphongo zija, ndi pa anaankhosa aja, malinga ndi chiŵerengero cha nyamazo ndi potsata malangizo ake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamodzi ndi ngʼombe zazimuna, nkhosa zazimuna ndi ana ankhosa, muzipereka zopereka za chakudya ndi za chakumwa molingana ndi chiwerengero cha nyamazo. |
Ndipo munthu akabwera nacho chopereka ndicho nsembe yaufa ya kwa Yehova, chopereka chake chizikhala cha ufa wosalala; ndipo athirepo mafuta, ndi kuikapo lubani.
Ndipo mubwere nao pamodzi ndi mikate, anaankhosa asanu ndi awiri, opanda chilema a chaka chimodzi, ndi ng'ombe yamphongo imodzi, ndi nkhosa zamphongo ziwiri; zikhale nsembe yopsereza ya Yehova, pamodzi ndi nsembe yao yaufa, ndi nsembe zao zothira, ndizo nsembe yamoto ya fungo lokoma la Yehova.
Ndipo nsembe zake zothira ndizo: limodzi la magawo khumi la hini wa vinyo ndiwo wa ng'ombe imodzi, ndi limodzi la magawo atatu la hini likhale la nkhosa yamphongo, ndi limodzi la magawo anai a hini likhale la mwanawankhosa; ndiyo nsembe yopsereza ya mwezi uliwonse kunena miyezi yonse ya chaka.
Ndi nsembe yake yothira ya mwanawankhosa mmodziyo ndiyo limodzi la magawo anai la hini; m'malo opatulika uthirire Yehova nsembe yothira ya chakumwa cholimba.
pamodzi ndi nsembe yopsereza ya pamwezi, ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira, monga mwa lemba lake, zikhale za fungo lokoma, nsembe yamoto ya Yehova.