Numeri 29:16 - Buku Lopatulika ndi tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, nsembe yake yaufa, ndi nsembe yake yothira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndi tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, nsembe yake yaufa, ndi nsembe yake yothira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Muperekenso tonde mmodzi kuti akhale nsembe yopepesera machimo, kuwonjezera pa nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku zija, pamodzi ndi chopereka cha chakudya ndi cha chakumwa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Muziperekanso mbuzi yayimuna imodzi kuti izikhale nsembe yopepesera machimo, kuwonjezera pa nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku zija pamodzi ndi chopereka chake cha chakudya ndi chakumwa. |
ndi pa mwanawankhosa mmodziyo pakhale limodzi la magawo khumi la ufa wosalala, wosakaniza ndi limodzi la magawo anai la hini wa mafuta opera; ndi limodzi la magawo anai la hini wa vinyo, likhale nsembe yothira.
akamdziwitsa kuchimwa kwake adachimwako, azidza nacho chopereka chake, ndicho tonde wopanda chilema;
ndiyo nsembe yopsereza ya tsiku la Sabata lililonse, pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yake yothira.
Ndi tonde mmodzi, akhale nsembe yauchimo ya Yehova; aikonze pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yake yothira.
Ndipo unene nao, Nsembe yamoto imene muzibwera nayo kwa Yehova ndiyi: anaankhosa awiri a chaka chimodzi opanda chilema, tsiku ndi tsiku, nsembe yamoto yosalekeza.
ndi limodzi la magawo khumi likhale la mwanawankhosa mmodzi, momwemo nao anaankhosa khumi ndi anai;