Nachita chikondwerero cha Misasa monga kwalembedwa, napereka nsembe yopsereza tsiku ndi tsiku mawerengedwe ake, monga mwa lamulo lake la tsiku lake pa tsiku lake;
Numeri 29:13 - Buku Lopatulika ndipo mubwere nayo nsembe yopsereza, ndiyo nsembe yamoto, ya fungo lokoma kwa Yehova: ng'ombe zamphongo khumi ndi zitatu, nkhosa zamphongo ziwiri, anaankhosa khumi ndi anai, a chaka chimodzi, akhale opanda chilema; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo mubwere nayo nsembe yopsereza, ndiyo nsembe yamoto, ya fungo lokoma kwa Yehova: ng'ombe zamphongo khumi ndi zitatu, nkhosa zamphongo ziwiri, anaankhosa khumi ndi anai, a chaka chimodzi, akhale opanda chilema; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pa tsiku loyamba mupereke nsembe yopsereza, nsembe yotentha pa moto, yotulutsa fungo lokomera Chauta. Ikhale ya anaang'ombe khumi ndi atatu amphongo, nkhosa ziŵiri zamphongo, anaankhosa khumi ndi anai amphongo a chaka chimodzi. Nyama zonsezo zikhale zopanda chilema. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Muzipereka nsembe yotentha pa moto, kuti izikhala fungo lokoma kwa Yehova, nsembe yopsereza ya ana angʼombe aamuna khumi ndi atatu, nkhosa zazimuna ziwiri, ndi ana ankhosa aamuna khumi ndi anayi a chaka chimodzi, zonse zopanda chilema. |
Nachita chikondwerero cha Misasa monga kwalembedwa, napereka nsembe yopsereza tsiku ndi tsiku mawerengedwe ake, monga mwa lamulo lake la tsiku lake pa tsiku lake;
Chopereka chake chikakhala nsembe yopsereza ya ng'ombe, azibwera nayo yaimuna yopanda chilema; abwere nayo ku khomo la chihema chokomanako, kuti alandirike pamaso pa Yehova.
Ndipo poyamba miyezi yanu muzibwera nayo nsembe yopsereza ya Yehova: ng'ombe zamphongo ziwiri, ndi nkhosa yamphongo imodzi, ndi anaankhosa asanu ndi awiri a chaka chimodzi opanda chilema;
koma mubwere nayo nsembe yamoto, nsembe yopsereza ya Yehova; ng'ombe ziwiri zamphongo, ndi nkhosa yamphongo imodzi, ndi anaankhosa asanu ndi awiri a chaka chimodzi; akhale kwa inu opanda chilema;
Pamenepo muzipereka nsembe yopsereza ya fungo lokoma kwa Yehova; ng'ombe zamphongo ziwiri, nkhosa yamphongo imodzi, anaankhosa asanu ndi awiri a chaka chimodzi;
Ndipo tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi wachisanu ndi chiwiri muzikhala nako kusonkhana kopatulika; musamachita ntchito ya masiku ena, koma muchitire Yehova madyerero masiku asanu ndi awiri;
ndi nsembe yake yaufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, atatu a magawo khumi akhale a efa wa ng'ombe imodzi, momwemo nazo ng'ombe khumi ndi zitatuzo, awiri a magawo khumi akhale a nkhosa yamphongo imodzi, momwemo nazo nkhosa zamphongo ziwirizo;
Pamenepo muzipereka nsembe yopsereza ya fungo lokoma kwa Yehova; ng'ombe imodzi yamphongo, nkhosa yamphongo imodzi, anaankhosa asanu ndi awiri a chaka chimodzi opanda chilema;
koma mubwere nayo nsembe yopsereza kwa Yehova, ya fungo lokoma; ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, anaankhosa asanu ndi awiri a chaka chimodzi; akhale kwa inu opanda chilema;
Chifukwa chake ndikupemphani inu, abale, mwa zifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera.