Koma atsuke ndi madzi matumbo ndi miyendo; ndi wansembe abwere nazo zonse nazitenthe paguwa la nsembe; ndiyo nsembe yopsereza, nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova.
Numeri 28:8 - Buku Lopatulika Ndi mwanawankhosa winayo umpereke madzulo; monga nsembe yaufa ya m'mawa, ndi nsembe yothira yake, umpereke; ndiyo nsembe yamoto ya fungo lokoma la Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndi mwanawankhosa winayo umpereke madzulo; monga nsembe yaufa ya m'mawa, ndi nsembe yothira yake, umpereke; ndiyo nsembe yamoto ya fungo lokoma la Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mwanawankhosa wina uja muzimpereka madzulo, pamodzi ndi chopereka cha chakudya ndi cha chakumwa zonga zam'maŵa zija. Imeneyi ikhalenso nsembe yotentha pa moto, yotulutsa fungo lokomera Chauta. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Muzipereka mwana wankhosa winayo madzulo, pamodzi ndi chopereka chachakudya monga poyamba paja ndi chopereka chachakumwa monga mmawa. Ichi ndi chopereka chachakudya, fungo lokoma kwa Yehova.’ ” |
Koma atsuke ndi madzi matumbo ndi miyendo; ndi wansembe abwere nazo zonse nazitenthe paguwa la nsembe; ndiyo nsembe yopsereza, nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova.
nang'ambe mapiko ake osawachotsa konse ai; ndipo wansembeyo aitenthe paguwa la nsembe, pa nkhuni zili pamoto; ndiyo nsembe yopsereza, nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova.
koma atsuke ndi madzi matumbo ake ndi miyendo yake; ndi wansembe atenthe zonsezi paguwa la nsembe, zikhale nsembe yopsereza, nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova.
Ndi nsembe yake yothira ya mwanawankhosa mmodziyo ndiyo limodzi la magawo anai la hini; m'malo opatulika uthirire Yehova nsembe yothira ya chakumwa cholimba.
Ndipo tsiku la Sabata anaankhosa awiri a chaka chimodzi, opanda chilema, ndi awiri a magawo khumi a efa wa ufa wosalala, ukhale nsembe yaufa, wosakaniza ndi mafuta, ndi nsembe yake yothira;
ndi tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira.