Ndipo anachotsapo nsembe zopsereza, kuti azipereke kwa ana a anthu monga mwa magawidwe a nyumba za makolo; azipereke kwa Yehova monga mulembedwa m'buku la Mose. Natero momwemo ndi ng'ombezo.
Numeri 28:31 - Buku Lopatulika Mupereke izi pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yake yaufa, zikhale kwa inu zopanda chilema, ndi nsembe zake zothira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mupereke izi pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yake yaufa, zikhale kwa inu zopanda chilema, ndi nsembe zake zothira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mupereke zimenezi pamodzi ndi zopereka za chakumwa, kuwonjezera pa nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku zija ndi chopereka cha chakudya. Musamale kuti nyamazo zikhale zopanda chilema. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Muzipereka zimenezi pamodzi ndi zopereka za zakumwa ndi nsembe yake ya chakudya. Onetsetsani kuti nyamazo zilibe chilema. |
Ndipo anachotsapo nsembe zopsereza, kuti azipereke kwa ana a anthu monga mwa magawidwe a nyumba za makolo; azipereke kwa Yehova monga mulembedwa m'buku la Mose. Natero momwemo ndi ng'ombezo.
Chopereka chake chikakhala nsembe yopsereza ya ng'ombe, azibwera nayo yaimuna yopanda chilema; abwere nayo ku khomo la chihema chokomanako, kuti alandirike pamaso pa Yehova.
koma mubwere nayo nsembe yamoto, nsembe yopsereza ya Yehova; ng'ombe ziwiri zamphongo, ndi nkhosa yamphongo imodzi, ndi anaankhosa asanu ndi awiri a chaka chimodzi; akhale kwa inu opanda chilema;
Ndipo unene nao, Nsembe yamoto imene muzibwera nayo kwa Yehova ndiyi: anaankhosa awiri a chaka chimodzi opanda chilema, tsiku ndi tsiku, nsembe yamoto yosalekeza.