Numeri 28:30 - Buku Lopatulika tonde mmodzi wakutetezera inu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 tonde mmodzi wakutetezera inu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Muperekenso tonde mmodzi wochitira mwambo wopepesera machimo anu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Muziperekanso mbuzi yayimuna imodzi kuti izikhala nsembe yopepesera machimo anu. |
Mukonzenso mwanawambuzi mmodzi akhale nsembe yauchimo, ndi anaankhosa awiri a chaka chimodzi akhale nsembe yoyamika.
pamenepo kudzali, ngati anachichita osati dala, osachidziwa khamulo, khamu lonse lipereke ng'ombe yamphongo ikhale nsembe yopsereza, ya fungo lokoma ya Yehova, pamodzi ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe yake yothira, monga mwa chiweruzo chake; ndi tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo.
Ndi tonde mmodzi, akhale nsembe yauchimo ya Yehova; aikonze pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yake yothira.
limodzi la magawo khumi likhale la mwanawankhosa mmodzi, momwemo ndi anaankhosa asanu ndi awiri;
Mupereke izi pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yake yaufa, zikhale kwa inu zopanda chilema, ndi nsembe zake zothira.
Ameneyo sanadziwe uchimo anamyesera uchimo m'malo mwathu; kuti ife tikhale chilungamo cha Mulungu mwa Iye.
Khristu anatiombola ku temberero la chilamulo, atakhala temberero m'malo mwathu; pakuti kwalembedwa, Wotembereredwa aliyense wopachikidwa pamtengo.
amene anasenza machimo athu mwini yekha m'thupi mwake pamtanda, kuti ife, titafa kumachimo, tikakhale ndi moyo kutsata chilungamo; ameneyo mikwingwirima yake munachiritsidwa nayo.
Pakuti Khristunso adamva zowawa kamodzi, chifukwa cha machimo, wolungama m'malo mwa osalungama, kuti akatifikitse kwa Mulungu; wophedwatu m'thupi, koma wopatsidwa moyo mumzimu;