Ndipo tsiku loyamba kukhale kusonkhana kopatulika, ndi tsiku lachisanu ndi chiwiri kukhalenso kusonkhana kopatulika; pasachitike ntchito masikuwo, zokhazi zakudya anthu onse ndizo muzichita.
Numeri 28:25 - Buku Lopatulika Ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri mukhale nako kusonkhana kopatulika; musamachita ntchito ya masiku ena. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri mukhale nako kusonkhana kopatulika; musamachita ntchito ya masiku ena. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri muchite msonkhano wopatulika. Musagwire ntchito zotopetsa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri muzichita msonkhano wopatulika ndipo musamagwire ntchito iliyonse. |
Ndipo tsiku loyamba kukhale kusonkhana kopatulika, ndi tsiku lachisanu ndi chiwiri kukhalenso kusonkhana kopatulika; pasachitike ntchito masikuwo, zokhazi zakudya anthu onse ndizo muzichita.
Masiku asanu ndi awiri uzikadya mkate wopanda chotupitsa, ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri likhale la madyerero a Yehova;
Ndipo mulalikire tsiku lomwelo; kuti mukhale nao msonkhano wopatulika; musamagwira ntchito ya masiku ena; ndilo lemba losatha m'nyumba zanu zonse, mwa mibadwo yanu yonse.
Masiku asanu ndi limodzi azigwira ntchito; koma lachisanu ndi chiwiri ndilo Sabata lakupumula, msonkhano wopatulika; musamagwira ntchito konse; ndilo Sabata la Yehova m'nyumba zanu zonse.
Tsiku lake loyamba mukhale nao msonkhano wopatulika; musamagwira ntchito ya masiku ena.
Koma mubwere nayo kwa Yehova nsembe yamoto masiku asanu ndi awiri; pa tsiku lachisanu ndi chiwiri pakhale msonkhano wopatulika; musamachita ntchito ya masiku ena.
Momwemonso tsiku la zipatso zoyamba, pobwera nayo nsembe ya ufa watsopano kwa Yehova, m'chikondwerero chanu cha Masabata, muzikhala nako kusonkhana kopatulika; musamachita ntchito ya masiku ena.
Ndipo mwezi wachisanu ndi chiwiri, tsiku loyamba la mweziwo, muzikhala nako kusonkhana kopatulika; musamachita ntchito ya masiku ena; likukhalireni inu tsiku lakuliza malipenga.
Ndipo tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi wachisanu ndi chiwiri muzikhala nako kusonkhana kopatulika; musamachita ntchito ya masiku ena, koma muchitire Yehova madyerero masiku asanu ndi awiri;
Tsiku lachisanu ndi chitatu muzikhala nalo tsiku loletsa; musamachita ntchito ya masiku ena;
Masiku asanu ndi limodzi muzidya mkate wopanda chotupitsa; ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri ndilo loletsa, la Yehova Mulungu wanu; musamagwira ntchito pamenepo.