Ndipo atulukire guwa la nsembe lokhala pamaso pa Yehova ndi kulichitira chotetezera; natengeko mwazi wa ng'ombeyo, ndi mwazi wa mbuziyo, ndi kuupaka pa nyanga za guwa la nsembe pozungulira.
Numeri 28:22 - Buku Lopatulika ndi tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo, yakutetezera inu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndi tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo, yakutetezera inu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Muperekenso tonde mmodzi kuti akhale nsembe yochitira mwambo wopepesera machimo anu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Muziphatikizapo mbuzi yayimuna monga nsembe yopepesera machimo anu. |
Ndipo atulukire guwa la nsembe lokhala pamaso pa Yehova ndi kulichitira chotetezera; natengeko mwazi wa ng'ombeyo, ndi mwazi wa mbuziyo, ndi kuupaka pa nyanga za guwa la nsembe pozungulira.
upereke limodzi la magawo khumi likhale la mwanawankhosa mmodzi; uzitero ndi anaankhosa asanu ndi awiri;
Pakuti chimene chilamulo sichinathe kuchita, popeza chinafooka mwa thupi, Mulungu anatumiza Mwana wake wa Iye yekha m'chifanizo cha thupi la uchimo, ndi chifukwa cha uchimo, natsutsa uchimo m'thupi;
koma pokwaniridwa nthawi, Mulungu anatuma Mwana wake, wobadwa ndi mkazi, wobadwa wakumvera lamulo,