Ndipo tsiku loyamba kukhale kusonkhana kopatulika, ndi tsiku lachisanu ndi chiwiri kukhalenso kusonkhana kopatulika; pasachitike ntchito masikuwo, zokhazi zakudya anthu onse ndizo muzichita.
Numeri 28:18 - Buku Lopatulika Tsiku loyamba pali kusonkhana kopatulika; musamachita ntchito ya masiku ena; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tsiku loyamba pali kusonkhana kopatulika; musamachita ntchito ya masiku ena; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pa tsiku loyamba pazikhala msonkhano wopatulika. Musagwire ntchito yotopetsa, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pa tsiku loyamba muzichita msonkhano wopatulika ndipo musamagwire ntchito iliyonse. |
Ndipo tsiku loyamba kukhale kusonkhana kopatulika, ndi tsiku lachisanu ndi chiwiri kukhalenso kusonkhana kopatulika; pasachitike ntchito masikuwo, zokhazi zakudya anthu onse ndizo muzichita.
Ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri mukhale nako kusonkhana kopatulika; musamachita ntchito ya masiku ena.
Momwemonso tsiku la zipatso zoyamba, pobwera nayo nsembe ya ufa watsopano kwa Yehova, m'chikondwerero chanu cha Masabata, muzikhala nako kusonkhana kopatulika; musamachita ntchito ya masiku ena.