Masiku asanu ndi awiri uzikadya mkate wopanda chotupitsa, ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri likhale la madyerero a Yehova;
Numeri 28:17 - Buku Lopatulika Ndipo tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi uwu pali zikondwerero; masiku asanu ndi awiri azidya mkate wopanda chotupitsa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi uwu pali zikondwerero; masiku asanu ndi awiri azidya mkate wopanda chotupitsa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo pa tsiku la 15 la mwezi umenewu, ndi tsiku lachikondwerero. Azidya buledi wosafufumitsa masiku asanu ndi aŵiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pa tsiku la 15 la mwezi womwewo pazikhala chikondwerero. Muzidya buledi wopanda yisiti kwa masiku asanu ndi awiri. |
Masiku asanu ndi awiri uzikadya mkate wopanda chotupitsa, ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri likhale la madyerero a Yehova;
Uzisunga chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa; masiku asanu ndi awiri uzidya mkate wopanda chotupitsa, monga ndinakuuza, nyengo yoikika, mwezi wa Abibu, pakuti m'menemo unatuluka mu Ejipito; koma asaoneke munthu pamaso panga opanda kanthu;
Uzisunga chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa. Uzidya mkate wopanda chotupitsa masiku asanu ndi awiri, monga ndakuuza pa nthawi yonenedwa, m'mwezi wa Abibu; pakuti mwezi wa Abibu unatuluka mu Ejipito.
Ndipo tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi womwewo ndilo chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa a Yehova; masiku asanu ndi awiri muzidya mkate wopanda chotupitsa.