Nakonze nsembe yaufa, kung'ombe kukhale efa; ndi kunkhosa yamphongo kukhale efa; ndi kuefa kukhale hini wa mafuta.
Numeri 28:12 - Buku Lopatulika ndi atatu a magawo khumi a efa wa ufa wosalala, ikhale nsembe yaufa, wosakaniza ndi mafuta, ndiwo wa ng'ombe iliyonse; ndi awiri a magawo khumi a ufa wosalala, ikhale nsembe yaufa, wosakaniza ndi mafuta, ndiwo wa nkhosa yamphongo imodziyo; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndi atatu a magawo khumi a efa wa ufa wosalala, ikhale nsembe yaufa, wosanganiza ndi mafuta, ndiwo wa ng'ombe iliyonse; ndi awiri a magawo khumi a ufa wosalala, ikhale nsembe yaufa, wosanganiza ndi mafuta, ndiwo wa nkhosa yamphongo imodziyo; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chopereka cha chakudya ikhale ya ufa wosalala wa makilogaramu atatu, wosakaniza ndi mafuta, pa ng'ombe yamphongo iliyonse. Muperekenso makilogaramu aŵiri a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, pa nkhosa yamphongoyo, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pa ngʼombe yayimuna iliyonse pakhale chopereka cha chakudya cha makilogalamu atatu a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta; ndi nkhosa yayimuna, chopereka cha chakudya cha makilogalamu awiri a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta; |
Nakonze nsembe yaufa, kung'ombe kukhale efa; ndi kunkhosa yamphongo kukhale efa; ndi kuefa kukhale hini wa mafuta.
Ndipo ana a Aroni azitenthe paguwa la nsembe, pa nsembe yopsereza, ili pa nkhuni zimene zili pamoto; ndiyo nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova.
ndi limodzi la magawo khumi la ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, ikhale nsembe yaufa, ndiwo wa mwanawankhosa yense; ndiyo nsembe yopsereza ya fungo lokoma, nsembe yamoto ya Yehova.
limodzi la magawo khumi likhale la mwanawankhosa mmodzi, momwemo ndi anaankhosa asanu ndi awiri;