Ndipo Amuramu anadzitengera Yokebede mlongo wa atate wake akhale mkazi wake; ndipo anambalira Aroni ndi Mose; ndi zaka za moyo wa Amuramu ndizo zana limodzi mphambu makumi atatu kudza zisanu ndi ziwiri.
Numeri 26:58 - Buku Lopatulika Awa ndi mabanja a Alevi: banja la Alibini, banja la Ahebroni, banja la Amali, banja la Amusi, banja la Akora. Ndipo Kohati anabala Amuramu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Awa ndi mabanja a Alevi: banja la Alibini, banja la Ahebroni, banja la Amali, banja la Amusi, banja la Akora. Ndipo Kohati anabala Amuramu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mabanja a Alevi anali aŵa: banja la Alibini, banja la Ahebroni, banja la Amahali, banja la Amusi, banja la Akora. Kohati anali bambo wa Amuramu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Awanso anali mabanja a Alevi: banja la Alibini, banja la Ahebroni, banja la Amali, banja la Amusi, fuko la Kora banja la Akohati, (Kohati anali abambo a Amramu. |
Ndipo Amuramu anadzitengera Yokebede mlongo wa atate wake akhale mkazi wake; ndipo anambalira Aroni ndi Mose; ndi zaka za moyo wa Amuramu ndizo zana limodzi mphambu makumi atatu kudza zisanu ndi ziwiri.
Ndipo ana aamuna a Kora ndiwo: Asiri ndi Elikana, ndi Abiyasafu; amenewo ndiwo mabanja a Akora.
Koma Kora, mwana wa Izihara, mwana wa Kohati, mwana wa Levi, anatenga Datani ndi Abiramu, ana a Eliyabu, ndi Oni mwana wa Peleti, ana a Rubeni;
Banja la Aamuramu, ndi banja la Aizihara, ndi banja la Ahebroni, ndi banja la Auziyele ndiwo a Kohati; ndiwo mabanja a Akohati.