Ndipo kudzachitika kuti muligawe ndi kuchita maere, likhale cholowa chanu, ndi cha alendo akukhala pakati pa inu; ndipo akhale kwa inu ngati obadwa m'dziko mwa ana a Israele, alandire cholowa pamodzi ndi inu mwa mafuko a Israele.
Numeri 26:56 - Buku Lopatulika Agawire ochuluka ndi ochepa cholowa chao monga mwa kuchita maere. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Agawire ochuluka ndi ochepa cholowa chao monga mwa kuchita maere. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choloŵa chaocho, uchigaŵe pakati pa fuko lalikulu ndi laling'ono mwamaere.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Cholowa chawo uchigawe pakati pa fuko lalikulu ndi lalingʼono mwa maere.” |
Ndipo kudzachitika kuti muligawe ndi kuchita maere, likhale cholowa chanu, ndi cha alendo akukhala pakati pa inu; ndipo akhale kwa inu ngati obadwa m'dziko mwa ana a Israele, alandire cholowa pamodzi ndi inu mwa mafuko a Israele.
Koma aligawe ndi kuchita maere; cholowa chao chikhale monga mwa maina a mafuko a makolo ao.
Ndipo awa ndi owerengedwa ao a Alevi monga mwa mabanja ao: Geresoni, ndiye kholo la banja la Ageresoni; Kohati, ndiye kholo la banja la Akohati; Merari, ndiye kholo la banja la Amerari.
Ndipo chiyani tsono? Ichi chimene Israele afunafuna sanachipeze; koma osankhidwawo anachipeza, ndipo otsalawo anaumitsidwa mtima;