Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Numeri 26:28 - Buku Lopatulika

Ana aamuna a Yosefe monga mwa mabanja ao ndiwo: Manase ndi Efuremu.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ana amuna a Yosefe monga mwa mabanja ao ndiwo: Manase ndi Efuremu.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Potsata mabanja ao ana aamuna a Yosefe anali aŵa: Manase ndi Efuremu.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Zidzukulu za Yosefe mwa mafuko awo kupyolera mwa Manase ndi Efereimu zinali izi:

Onani mutuwo



Numeri 26:28
9 Mawu Ofanana  

Kwa Yosefe kunabadwa m'dziko la Ejipito Manase ndi Efuremu, amene Asenati mwana wamkazi wa Potifera wansembe wa Oni anambalira iye.


Tsopano ana ako aamuna awiri, amene anakubadwira iwe m'dziko la Ejipito, ndisanadze kwa iwe ku Ejipito, ndiwo anga; Efuremu ndi Manase, monga Rubeni ndi Simeoni, ndiwo anga.


Ndi anthu a hafu la fuko la Manase anakhala m'dziko; anachuluka kuyambira Basani kufikira Baala-Heremoni, ndi Seniri, ndi phiri la Heremoni.


Ana a Manase ndiwo Asiriele amene mkazi wake anambala. Koma mkazi wake wamng'ono Mwaramu anabala Makiri atate wa Giliyadi;


A ana a Manase, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;


ndi zinthu zofunikatu za dziko lapansi, ndi kudzala kwake, ndi chivomerezo cha Iye anakhala m'chitsambayo. Mdalitso ufike pamutu wa Yosefe, ndi pakati pamutu wake wa iye wokhala padera ndi abale ake.


Pakuti ana a Yosefe ndiwo mafuko awiri, Manase ndi Efuremu; ndipo sanawagawire Alevi kanthu m'dziko, koma mizinda yokhalamo ndi dziko lozungulirako likhale la zoweta zao ndi chuma chao.