Ndipo Mowabu anati kwa akulu a Midiyani, Tsopano msonkhano uwu udzanyambita zonse zili pozinga pathu, monga ng'ombe zinyambita msipu wa kubusa. Ndipo Balaki mwana wa Zipori anali mfumu ya Mowabu masiku amenewo.
Numeri 25:17 - Buku Lopatulika Sautsa Amidiyani ndi kuwakantha; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Sautsa Amidiyani ndi kuwakantha; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Uŵathire nkhondo Amidiyani, ndiponso uŵaononge Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Amidiyani ndi adani anu ndipo uwaphe, |
Ndipo Mowabu anati kwa akulu a Midiyani, Tsopano msonkhano uwu udzanyambita zonse zili pozinga pathu, monga ng'ombe zinyambita msipu wa kubusa. Ndipo Balaki mwana wa Zipori anali mfumu ya Mowabu masiku amenewo.
Ndipo Israele anakhala mu Sitimu, ndipo anthu anayamba kuchita chigololo ndi ana aakazi a Mowabu;
popeza akusautsani ndi manyengo ao amene anakunyengani nao; m'chija cha Peori, ndi cha Kozibi, mwana wamkazi wa kalonga wa ku Midiyani, mlongo wao, amene adamupha tsiku la mliri, m'chija cha Peori.
Muubwezere, monganso uwu unabwezera, ndipo muwirikize kawiri, monga mwa ntchito zake; m'chikhomo unathiramo, muuthirire chowirikiza.
Koma ana a Israele anachita choipa pamaso pa Yehova; ndipo Yehova anawapereka m'dzanja la Midiyani zaka zisanu ndi ziwiri.