Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Numeri 25:12 - Buku Lopatulika

Chifukwa chake nena, Taonani, ndimpatsa iye pangano langa la mtendere;

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Chifukwa chake nena, Taonani, ndimpatsa iye pangano langa la mtendere;

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Motero umuuze kuti ndikupangana naye tsopano chipangano chamtendere.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Tsono muwuze kuti ndikhazikitsa pangano langa la mtendere ndi iye.

Onani mutuwo



Numeri 25:12
9 Mawu Ofanana  

Pamenepo panauka Finehasi, nachita chilango: Ndi mliriwo unaletseka.


Ndipo adamuyesa iye wachilungamo, ku mibadwomibadwo kunthawi zonse.


Pakuti mapiri adzachoka, ndi zitunda zidzasunthika; koma kukoma mtima kwanga sikudzakuchokera iwe, kapena kusunthika chipangano changa cha mtendere, ati Yehova amene wakuchitira iwe chifundo.


Ndipo ndidzapangana nazo pangano la mtendere, ndi kuleketsa zilombo zoipa m'dzikomo; ndipo zidzakhala mosatekeseka m'chipululu, ndi kugona kunkhalango.


Ndipo ndidzapangana nao pangano la mtendere, lidzakhala pangano losatha nao, ndipo ndidzawakhazika, ndi kuwachulukitsa, ndi kuika malo anga opatulika pakati pao kosatha.


Koma inu mwapatuka m'njira; mwakhumudwitsa ambiri m'chilamulo; mwaipsa chipangano cha Levi, ati Yehova wa makamu.


Taonani, ndituma mthenga wanga, kuti akonzeretu njira pamaso panga; ndipo Ambuye amene mumfuna adzadza ku Kachisi wake modzidzimutsa; ndiye mthenga wa chipangano amene mukondwera naye; taonani akudza, ati Yehova wa makamu.


Aamaleke akhala m'dziko la kumwera; ndi Ahiti, ndi Ayebusi, ndi Aamori, akhala ku mapiri, ndi Akanani akhala kunyanja, ndi m'mphepete mwa Yordani.