Ndodo yachifumu siidzachoka mwa Yuda, kapena wolamulira pakati pa mapazi ake, kufikira atadza Silo; ndipo anthu adzamvera iye.
Numeri 24:19 - Buku Lopatulika Ndipo wina wotuluka mu Yakobo adzachita ufumu; nadzapasula otsalira m'mizinda. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo wina wotuluka m'Yakobo adzachita ufumu; nadzapasula otsalira m'mudzi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mwa Yakobe mudzatuluka mfumu yolamulira, imene idzaononga otsala mu mzinda.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Wolamulira adzachokera mwa Yakobo ndipo adzawononga otsala a mu mzindamo.” |
Ndodo yachifumu siidzachoka mwa Yuda, kapena wolamulira pakati pa mapazi ake, kufikira atadza Silo; ndipo anthu adzamvera iye.
Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti muzu wa Yese umene uima ngati mbendera ya mitundu ya anthu, amitundu adzafunafuna uwu; ndipo popuma pake padzakhala ulemerero.
Koma iwe, Betelehemu Efurata, ndiwe wamng'ono kuti ukhale mwa zikwi za Yuda, mwa iwe mudzanditulukira wina wakudzakhala woweruza mu Israele; matulukiro ake ndiwo a kale lomwe, kuyambira nthawi yosayamba.
Ndipo adzaimirira, nadzadyetsa nkhosa zake mu mphamvu ya Yehova, mu ukulu wa dzina la Yehova Mulungu wake; ndipo iwo adzakhalabe; pakuti pamenepo Iye adzakhala wamkulu kufikira malekezero a dziko lapansi.
Ndi Edomu adzakhala akeake, Seiri lomwe lidzakhala lakelake, ndiwo adani ake; koma Israele adzachita zamphamvu.
Ndipo anayang'ana ku Amaleke, nanena fanizo lake, nati, Amaleke ndiye woyamba wa amitundu; koma chitsiriziro chake, adzaonongeka ku nthawi zonse.
Ndipo amenewa adzachoka kunka ku chilango cha nthawi zonse; koma olungama kumoyo wa nthawi zonse.
Ndipo Yesu anadza nalankhula nao, nanena, Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi padziko lapansi.
Pamenepo anati, Munthu wa fuko lomveka ananka kudziko lakutali, kudzilandirira yekha ufumu, ndi kubwerako.
Koma adani anga aja osafuna kuti ndidzakhala mfumu yao, bwerani nao kuno, nimuwaphe pamaso panga.
Koma ponena za Mwana, ati, Mpando wachifumu wanu, Mulungu, ufikira nthawi za nthawi; ndipo ndodo yachifumu yoongoka ndiyo ndodo ya ufumu wanu.
amene akhala padzanja lamanja la Mulungu, atalowa mu Mwamba; pali angelo, ndi maulamuliro, ndi zimphamvu, zonse zimgonjera.
Ndipo ali nalo pa chovala chake ndi pa ntchafu yake dzina lolembedwa, MFUMU YA MAFUMU, NDI MBUYE WA AMBUYE.