Ndipo Balamu anayankha nati kwa anyamata a Balaki, Chinkana Balaki andipatsa nyumba yake yodzala ndi siliva ndi golide, sindikhoza kutumpha mau a Yehova Mulungu wanga, kuchepsako kapena kuonjezako.
Numeri 24:12 - Buku Lopatulika Ndipo Balamu anati kwa Balaki, Kodi sindinauzanso amithenga anu amene munawatumiza kwa ine, ndi kuti, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Balamu anati kwa Balaki, Kodi sindinauzanso amithenga anu amene munawatumiza kwa ine, ndi kuti, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Balamu adafunsa Balaki kuti “Kodi amithenga anu amene mudaŵatuma kwa ine aja, sindidaŵauze kuti, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Balaamu anayankha Balaki kuti, “Kodi sindinawawuze amithenga amene munawatumiza kwa ine, |
Ndipo Balamu anayankha nati kwa anyamata a Balaki, Chinkana Balaki andipatsa nyumba yake yodzala ndi siliva ndi golide, sindikhoza kutumpha mau a Yehova Mulungu wanga, kuchepsako kapena kuonjezako.
Ndipo Balamu anati kwa Balaki, Taonani, ndafika kwa inu; ngati ndili nayo mphamvu konse tsopano kunena kanthu? Mau amene Mulungu aike m'kamwa mwanga ndiwo ndidzanena.
Chifukwa chake thawira ku malo ako tsopano; ndikadakuchitira ulemu waukulu; koma, taona, Yehova wakuletsera ulemu.