Ndipo popeza Mulungu anathandiza Alevi akusenza likasa la chipangano la Yehova, iwo anapha nsembe ng'ombe zisanu ndi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri.
Numeri 23:29 - Buku Lopatulika Ndipo Balamu anati kwa Balaki, Mundimangire pano maguwa a nsembe asanu ndi awiri, nimundikonzere pano ng'ombe zisanu ndi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Balamu anati kwa Balaki, Mundimangire pano maguwa a nsembe asanu ndi awiri, nimundikonzere pano ng'ombe zisanu ndi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Balamu adauza Balaki kuti, “Mundimangire maguwa asanu ndi aŵiri pano, ndipo mundikonzere ng'ombe zamphongo zisanu ndi ziŵiri ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziŵiri.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Balaamu anati kwa Balaki, “Mundimangire maguwa ansembe asanu ndi awiri pano ndipo mundikonzere ngʼombe zazimuna zisanu ndi ziwiri, nkhosa zazimuna zisanu ndi ziwiri.” |
Ndipo popeza Mulungu anathandiza Alevi akusenza likasa la chipangano la Yehova, iwo anapha nsembe ng'ombe zisanu ndi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri.
Ndipo Balaki anachita monga adanena Balamu, napereka ng'ombe ndi nkhosa yamphongo paguwa la nsembe lililonse.