Koma Iye ndiye wa mtima umodzi, adzambweza ndani? Ndi ichi chimene moyo wake uchifuna achichita.
Numeri 23:27 - Buku Lopatulika Ndipo Balaki anati kwa Balamu, Tiyetu, ndimuke nawe kumalo kwina; kapena kudzakomera pamaso pa Mulungu kuti unditembererere iwo pokhala kumeneko. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Balaki anati kwa Balamu, Tiyetu, ndimuke nawe kumalo kwina; kapena kudzakomera pamaso pa Mulungu kuti unditembererere iwo pokhala kumeneko. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Balaki adauza Balamu kuti, “Tiyeni limodzi tipite ku malo ena. Mwina mwake zidzamkondwetsa Mulungu kuti muŵatemberere m'malo mwanga, mutaima pamenepo.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Balaki anati kwa Balaamu, “Bwera ndikutengere ku malo ena. Mwina chidzamukondweretsa Mulungu kuti uwatemberere kumeneko mʼmalo mwanga.” |
Koma Iye ndiye wa mtima umodzi, adzambweza ndani? Ndi ichi chimene moyo wake uchifuna achichita.
Pakuti Yehova wa makamu wapanga uphungu, ndani adzauleketsa? Ndi dzanja lake latambasulidwa, ndani adzalibweza?
Ndipo tsopano, idzatu, nunditembererere anthu awa; popeza andiposa mphamvu; kapena ndidzawapambana, kuti tiwakanthe, ndi kuti ndiwapirikitse m'dziko; pakuti ndidziwa kuti iye amene umdalitsa adalitsika, ndi iye amene umtemberera atemberereka.
Ndipo Balaki anati naye, Tiyetu, upite nane kumalo kwina, kumene ukawaona; udzaona malekezero ao okha, osawaona onse; ndipo pokhala pamenepo ukanditembererere iwo.
Koma Balamu anayankha nati kwa Balaki, Sindinakuuzani ndi kuti, Chilichonse achinena Yehova, chomwecho ndizichita?