ndipo ndidzakuyesa iwe mtundu waukulu, ndipo ndidzakudalitsa iwe, ndi kubukitsa dzina lako; nukhale iwe mdalitso;
Numeri 23:20 - Buku Lopatulika Kapena kulankhula, osachitsimikiza? Taonani, ndalandira mau akudalitsa, popeza Iye wadalitsa, sinditha kusintha. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kapena kulankhula, osachitsimikiza? Taonani, ndalandira mau akudalitsa, popeza Iye wadalitsa, sinditha kusintha. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndithu, ndalandira lamulo kuti ndidalitse. Iye wadalitsa, ndipo ine sindingathe kusintha kanthu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Wandilamula kuti ndidalitse, Iyeyo wadalitsa ndipo sindingasinthe. |
ndipo ndidzakuyesa iwe mtundu waukulu, ndipo ndidzakudalitsa iwe, ndi kubukitsa dzina lako; nukhale iwe mdalitso;
kudalitsa ndidzakudalitsa iwe, kuchulukitsa ndidzachulukitsa mbeu zako monga nyenyezi za kumwamba, monga mchenga wa m'mphepete mwa nyanja; ndipo mbeu zako zidzagonjetsa chipata cha adani ao;
Ndipo Isaki ananthunthumira ndi kunthunthumira kwakukulu, nati, Ndani uja anatenga nyama, nadza nayo kwa ine, ndipo ndadyako zonse usadalowe iwe, ndipo ndamdalitsa iye? Inde, adzadalitsika.
chakukomerani kudalitsa nyumba ya mtumiki wanu, kuti ikhalebe kosatha pamaso panu; pakuti Inu Yehova mwadalitsa, ndipo idzadalitsika kosatha.
Inde chiyambire nthawi Ine ndine, ndipo palibe wina wopulumutsa m'dzanja langa; ndidzagwira ntchito, ndipo ndani adzaletsa?
Ndipo Balamu anayankha nati kwa anyamata a Balaki, Chinkana Balaki andipatsa nyumba yake yodzala ndi siliva ndi golide, sindikhoza kutumpha mau a Yehova Mulungu wanga, kuchepsako kapena kuonjezako.
Ndipo Balamu anati kwa Balaki, Taonani, ndafika kwa inu; ngati ndili nayo mphamvu konse tsopano kunena kanthu? Mau amene Mulungu aike m'kamwa mwanga ndiwo ndidzanena.
amene musungidwa ndi mphamvu ya Mulungu mwa chikhulupiriro, kufikira chipulumutso chokonzeka kukavumbulutsidwa nthawi yotsiriza.