Ndipo anadza kuli iye, ndipo taona, analikuima pa nsembe yake yopsereza, ndi akalonga a Mowabu pamodzi naye. Ndipo Balaki anati kwa iye, Wanenanji Yehova?
Numeri 23:18 - Buku Lopatulika Ndipo ananena fanizo lake, nati, Ukani, Balaki, imvani; ndimvereni, mwana wa Zipori. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ananena fanizo lake, nati, Ukani, Balaki, imvani; ndimvereni, mwana wa Zipori. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo Balamu adayamba kulankhula mau auneneri, adati, “Dzukani, Balaki, ndipo mumve, mundimvere inu mwana wa Zipori. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamenepo Balaamu ananena uthenga wake: “Nyamuka Balaki ndipo tamvera; Undimvere iwe mwana wa Zipori. |
Ndipo anadza kuli iye, ndipo taona, analikuima pa nsembe yake yopsereza, ndi akalonga a Mowabu pamodzi naye. Ndipo Balaki anati kwa iye, Wanenanji Yehova?
Mulungu sindiye munthu, kuti aname; kapena mwana wa munthu, kuti aleke; kodi anena, osachita?
Ndipo Ehudi anamdzera alikukhala pa yekha m'chipinda chosanja chopitidwa mphepo. Nati Ehudi, Ndili nao mau a Mulungu akukuuzani. Nauka iye pa mpando wake.