Ndipo Yakobo anapereka nsembe paphiripo, naitana abale ake kuti adye chakudya; ndipo anadya chakudya, nagona paphiripo usiku wonse.
Numeri 22:40 - Buku Lopatulika Pamenepo Balaki anapha ng'ombe ndi nkhosa, natumizira Balamu, ndi akalonga okhala naye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo Balaki anapha ng'ombe ndi nkhosa, natumizira Balamu, ndi akalonga okhala naye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kumeneko Balaki adapereka nsembe ya ng'ombe ndi nkhosa, natumizako nyama kwa Balamu ndi kwa akalonga amene anali naye aja. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Balaki anapereka nsembe ngʼombe ndi nkhosa, ndipo anapereka zina kwa Balaamu ndi kwa akuluakulu omwe anali naye. |
Ndipo Yakobo anapereka nsembe paphiripo, naitana abale ake kuti adye chakudya; ndipo anadya chakudya, nagona paphiripo usiku wonse.
Ndipo kunali kuti m'mawa, Balaki anatenga Balamu, nakwera naye ku misanje ya Baala, ndi kumeneko anaona malekezero a anthuwo.
Ndipo anamuka naye ku thengo la Zofimu, pamwamba pa Pisiga, namangako maguwa a nsembe asanu ndi awiri, napereka ng'ombe ndi nkhosa yamphongo paguwa la nsembe lililonse.
Ndipo Balaki anachita monga Balamu ananena; ndipo Balaki ndi Balamu anapereka paguwa la nsembe lililonse ng'ombe ndi nkhosa yamphongo.
Ndipo Balaki anachita monga adanena Balamu, napereka ng'ombe ndi nkhosa yamphongo paguwa la nsembe lililonse.