Numeri 22:35 - Buku Lopatulika Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa Balamu, Pita nao anthuwa; koma mau okhaokha ndinena ndi iwe, ndiwo ukanene. Potero Balamu anamuka nao akalonga a Balaki. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa Balamu, Pita nao anthuwa; koma mau okhaokha ndinena ndi iwe, ndiwo ukanene. Potero Balamu anamuka nao akalonga a Balaki. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo mngelo wa Chauta adauza Balamu kuti, “Pita nawo anthuŵa. Koma ukanene zokhazo zimene ndikakuuze.” Choncho Balamu adapitirira ulendo wake pamodzi ndi akalonga a Balaki aja. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mngelo wa Yehova anati kwa Balaamu, “Pita ndi anthuwa koma ukayankhule zokhazo zimene ndikakuwuze.” Choncho Balaamu anapita ndi akuluakulu a Balaki. |
Pamene Balaki anamva kuti wafika Balamu, anamtulukira kukakomana naye kumzinda wa Mowabu, wokhala m'mphepete mwa Arinoni, ndiwo ku malekezero a malire ake.
koma sindinafuna kumvera Balamu, potero anakudalitsani chidalitsire, ndipo ndinakulanditsani m'dzanja lake.