Numeri 22:33 - Buku Lopatulika koma bulu anandiona, nandipatukira nthawi izi zitatu pondiona; akadapanda kundipatukira, ndikadakupha iwe ndithu, ndi kumsunga iye wamoyo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 koma bulu anandiona, nandipatukira nthawi izi zitatu pondiona; akadapanda kundipatukira, ndikadakupha iwe ndithu, ndi kumsunga iye wamoyo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Bulu wako anandiwona, ndipo anasiya njira katatu konse atandiwona. Akadapanda kusiya njira atandiwona, ndithu ndikadakuphera pomwepo, koma buluyo ndikadamleka kuti akhale moyo.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Buluyu anandiona ndi kupatuka katatu aka. Akanakhala kuti sanapatuke, ndikanakupha tsopano, koma buluyu nʼkanamusiya ndi moyo.” |
Ndipo mthenga wa Yehova ananena naye, Wapandiranji bulu wako katatu tsopano? Taona, ndatuluka kuti nditsutsane nawe popeza njira iyi ikugwetsa chamutu pamaso panga;
Pamenepo Balamu anati kwa mthenga wa Yehova, Ndachimwa, popeza sindinadziwe kuti munaima mondiletsa m'njira; ndipo tsopano, ngati chikuipirani, ndibwerera.