Koma Yehova ananena naye, Anampangira munthu m'kamwa ndani? Kapena analenga munthu wosalankhula ndani, kapena wogontha, kapena wamaso, kapena wakhungu? Si ndine Yehova kodi?
Numeri 22:28 - Buku Lopatulika Ndipo Yehova anatsegula pakamwa pake pa bulu, nati uyu kwa Balamu, Ndakuchitanji, kuti wandipanda katatu tsopano? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yehova anatsegula pakamwa pake pa bulu, nati uyu kwa Balamu, Ndakuchitanji, kuti wandipanda katatu tsopano? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo Chauta adatsekula pakamwa pa buluyo, ndipo adalankhula, nafunsa Balamu kuti, “Kodi ndakuchitani chiyani kuti muzindimenya chotere katatu?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamenepo Yehova anayankhulitsa bulu uja, ndipo buluyo anati kwa Balaamu, “Ndakuchitirani chiyani kuti mundimenye katatuka?” |
Koma Yehova ananena naye, Anampangira munthu m'kamwa ndani? Kapena analenga munthu wosalankhula ndani, kapena wogontha, kapena wamaso, kapena wakhungu? Si ndine Yehova kodi?
Pamenepo Balamu anati kwa bulu, Chifukwa wandipeputsa; mukadakhala lupanga m'dzanja langa tsopano, ndikadakupha iwe.
Pakuti tidziwa kuti cholengedwa chonse chibuula, ndi kugwidwa m'zowawa pamodzi kufikira tsopano.
Pakuti kulembedwa, Ndidzaononga nzeru za anzeru, ndi kuchenjera kwa ochenjera ndidzakutha.
koma anadzudzulidwa pa kulakwa kwake mwini; bulu wopanda mau, wolankhula ndi mau a munthu, analetsa kuyaluka kwa mneneriyo.