Ndipo Balamu anayankha nati kwa anyamata a Balaki, Chinkana Balaki andipatsa nyumba yake yodzala ndi siliva ndi golide, sindikhoza kutumpha mau a Yehova Mulungu wanga, kuchepsako kapena kuonjezako.
Numeri 22:19 - Buku Lopatulika Ndikupemphani, tsono, khalani pano inu usiku uno womwe; kuti ndidziwe chomwe Yehova adzanenanso nane. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndikupemphani, tsono, khalani pano inu usiku uno womwe; kuti ndidziwe chomwe Yehova adzanenanso nane. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndiye inu tsono, gonani konkuno usiku uno, monga adachitira anzanu aja, kuti ndidziŵe ngati pali zina zimene Chauta andiwuze.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsopano mukhale kuno usiku uno monga ena anachitira, ndidzaona chimene Yehova adzandiwuza.” |
Ndipo Balamu anayankha nati kwa anyamata a Balaki, Chinkana Balaki andipatsa nyumba yake yodzala ndi siliva ndi golide, sindikhoza kutumpha mau a Yehova Mulungu wanga, kuchepsako kapena kuonjezako.
Ndipo Mulungu anadza kwa Balamu usiku, nanena naye, Akadza kukuitana anthuwa, nyamuka, kunka nao, koma mau okhaokha ndinena ndi iwe, ndiwo ukachite.
posiya njira yolunjika, anasokera, atatsata njira ya Balamu mwana wa Beori, amene anakonda mphotho ya chosalungama;
Ndipo m'chisiriro adzakuyesani malonda ndi mau onyenga; amene chiweruzo chao sichinachedwe ndi kale lomwe, ndipo chitayiko chao sichiodzera.
Tsoka kwa iwo! Pakuti anayenda m'njira ya Kaini, ndipo anadziononga m'chisokero cha Balamu chifukwa cha kulipira, natayika m'chitsutsano cha Kora.