dzikoli Yehova analikantha pamaso pa gulu la Israele, ndilo dziko la zoweta ndipo anyamata anu ali nazo zoweta.
Numeri 21:35 - Buku Lopatulika Ndipo anamkantha iye, ndi ana ake aamuna ndi anthu ake onse, kufikira sanatsale ndi mmodzi yense; nalanda dziko lake likhale laolao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anamkantha iye, ndi ana ake amuna ndi anthu ake onse, kufikira sanatsale ndi mmodzi yense; nalanda dziko lake likhale laolao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho Aisraele adapha Ogi, ana ake aamuna ndi anthu ake onse, kotero kuti panalibe ndi mmodzi yemwe amene adatsalira, ndipo adalanda dziko lakelo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho Aisraeli anapha Ogi pamodzi ndi ana ake aamuna ndi gulu lake lonse la nkhondo. Palibe ndi mmodzi yemwe amene anatsala wamoyo, ndipo analanda dziko lakelo. |
dzikoli Yehova analikantha pamaso pa gulu la Israele, ndilo dziko la zoweta ndipo anyamata anu ali nazo zoweta.
Ndipo Ahori anakhala mu Seiri kale, koma ana a Esau analanda dziko lao, nawaononga pamaso pao, nakhala m'malo mwao; monga Israele anachitira dziko lakelake, limene Yehova anampatsa).
Ndipo Yehova adzawachitira monga anachitira Sihoni ndi Ogi, mafumu a Aamori, ndi dziko lao limene analiononga.
tsidya lija la Yordani, m'chigwa cha pandunji pa Betepeori, m'dziko la Sihoni mfumu ya Aamori, wakukhala mu Hesiboni, amene Mose ndi ana a Israele anamkantha, potuluka iwo mu Ejipito;
ndipo analanda dziko lake, ndi dziko la Ogi mfumu ya Basani, mafumu awiri a Aamori, akukhala tsidya lija la Yordani lotuluka dzuwa;
ufumu wonse wa Ogi mu Basani, wa kuchita ufumu mu Asitaroti, ndi mu Ederei (yemweyo anatsala pa otsala a Arefaimu); pakuti Mose anakantha awa, nawainga.
Ndipo Yehova anati kwa ana a Israele, Kodi sindinakupulumutsani kwa Aejipito ndi kwa Aamori, ndi kwa ana a Amoni, ndi kwa Afilisti?