Numeri 21:30 - Buku Lopatulika Tinawagwetsa; Hesiboni waonongeka kufikira ku Diboni, ndipo tinawapululutsa kufikira ku Nofa. Ndiwo wakufikira ku Medeba. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tinawagwetsa; Hesiboni waonongeka kufikira ku Diboni, ndipo tinawapululutsa kufikira ku Nofa. Ndiwo wakufikira ku Medeba. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho zidzukulu zao zidatha nkufa, kuyambira ku Hesiboni mpaka ku Diboni, ndipo tidaŵaononga mpaka ku Nofa, pafupi ndi Medeba.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Koma ife tawagonjetsa; Hesiboni wawonongedwa mʼnjira monse mpaka kufika ku Diboni. Tawaphwasula mpaka ku mzinda wa Nofa, mzinda womwe umafika ku Medeba. |
Ndipo akuponyawo amene anali palinga anaponya anyamata anu; ndipo anyamata ena a mfumu anafa, ndi mnyamata wanu Uriya Muhiti, iyenso anafa.
Momwemo anadzilembera magaleta zikwi makumi atatu mphambu ziwiri, ndi mfumu ya Maaka ndi anthu ake; nadza iwo, namanga misasa chakuno cha Medeba. Ana a Amoni omwe anasonkhana m'mizinda mwao, nadza kunkhondo.
Akwera ku Kachisi, ndi ku Diboni, kumisanje, kukalira; pa Nebo ndi pa Medeba a Mowabu pali kulira; pamitu pao ponse pali dazi, ndevu zonse zametedwa.
Pakuti madzi a Diboni adzala mwazi; pakuti ndidzatengera zina pa Diboni, mkango pa iye amene anapulumuka ku Mowabu, ndi pa otsala a m'dziko.
Iwe mwana wamkazi wokhala mu Diboni, utsike pa ulemerero wako, nukhale ndi ludzu; pakuti wakufunkha Mowabu wakukwerera, iwe waononga malinga ako.
Ataroti, ndi Diboni, ndi Yazere, ndi Nimira, ndi Hesiboni, ndi Eleyale, ndi Sibima, ndi Nebo, ndi Beoni,
Hesiboni ndi mizinda yake yonse yokhala pachidikha; Diboni, ndi Bamoti-Baala ndi Bete-Baala-Meoni;
kuyambira pa Aroere, wokhala m'mphepete mwa chigwa cha Arinoni, ndi mzinda uli pakati pa chigwa, ndi chidikha chonse cha Medeba mpaka ku Diboni;