Numeri 21:28 - Buku Lopatulika Popeza moto unatuluka mu Hesiboni, chirangali cha moto m'mzinda wa Sihoni; chatha Ari wa Mowabu, eni misanje ya Arinoni. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Popeza moto unatuluka m'Hesiboni, chirangali cha moto m'mudzi wa Sihoni; chatha Ari wa Mowabu, eni misanje ya Arinoni. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Moto udabuka ku Hesiboni. Malaŵi a moto adatuluka mu mzinda wa Sihoni. Moto udaononga Ari mzinda wa ku Mowabu, udapserezeratu mapiri a kumtunda kwa Arinoni. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Moto unabuka ku Hesiboni, malawi a moto kuchokera mu mzinda wa Sihoni. Unanyeketsa Ari mzinda wa ku Mowabu, nzika za ku malo okwera a Arinoni. |
Chifukwa chake Ambuye, Yehova wa makamu, adzatumiza kuonda mwa onenepa ake; ndipo pansi pa ulemerero wake padzayaka kutentha, konga ngati kutentha kwa moto.
Ndi Hesiboni afuula zolimba, ndi Eleyale; mau ao amveka, ngakhale ku Yahazi; chifukwa chake amuna ankhondo a Mowabu afuula zolimba; moyo wake wanthunthumira m'kati mwake.
Ndipo padzakhala kuti pamene Mowabu adzadzionetsa yekha, ndi kudzitopetsa pamsanje, ndipo kufika kumalo ake oyera kudzapemphera, sadzapindulapo kanthu.
koma ndidzayatsa moto pa linga la Raba, udzanyeketsa nyumba zachifumu zake, ndi kufuula tsiku la nkhondo, ndi namondwe, tsiku la kamvulumvulu;
koma ndidzatumiza moto kunyumba ya Hazaele, ndipo udzanyeketsa nyumba zachifumu za Benihadadi.
koma ndidzatumiza moto pa Mowabu, udzanyeketsa nyumba zachifumu za Keriyoti; ndipo Mowabu adzafa ndi phokoso, ndi kufuula, ndi mau a lipenga;
ndi zigwa za miyendoyo zakutsikira kwao kwa Ari, ndi kuyandikizana ndi malire a Mowabu.
Chifukwa chake iwo akunena mophiphiritsa akuti, Idzani ku Hesiboni, mzinda wa Sihoni umangike, nukhazikike.
Ndipo kunali kuti m'mawa, Balaki anatenga Balamu, nakwera naye ku misanje ya Baala, ndi kumeneko anaona malekezero a anthuwo.
Ndipo Yehova anati kwa ine, Usavuta Mowabu, kapena kuutsana naye nkhondo; popeza sindidzakupatsako dziko lake likhale lakolako; pakuti ndinapatsa ana a Loti Ari likhale laolao.
Ndipo nkandankhuku unati kwa mitengo, Mukandidzoza mfumu yanu moonadi, tiyeni, thawirani ku mthunzi wanga; mukapanda kutero utuluke moto m'nkandankhuku ndi kunyeketsa mikungudza ya Lebanoni.
koma ngati simunatero, utuluke moto kwa Abimeleki, nunyeketse eni ake a ku Sekemu ndi nyumba ya Milo; nutuluke moto kwa eni ake a ku Sekemu, ndi kunyumba yake ya Milo, nunyeketse Abimeleki.