Numeri 20:28 - Buku Lopatulika Ndipo Mose anavula Aroni zovala zake, naveka Eleazara mwana wake; ndipo Aroni anafa pomwepo pamwamba paphiri. Pamenepo Mose ndi Eleazara anatsika m'phirimo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mose anavula Aroni zovala zake, naveka Eleazara mwana wake; ndipo Aroni anafa pomwepo pamwamba pa phiri. Pamenepo Mose ndi Eleazara anatsika m'phirimo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo Mose adamuvula Aroni zovala zake zaunsembe, naveka Eleazara mwana wake. Ndipo Aroni adafera pamwamba pa phiri pomwepo. Tsono Mose ndi Eleazara adatsika phiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamenepo Mose anavula Aaroni zovala zake ndi kuveka mwana wake Eliezara. Aaroni anafa kumeneko pamwamba pa phirilo. Koma Mose ndi Eliezara anatsika ku phiriko, |
ndipo zikhale za Aroni ndi za ana ake aamuna, mwa lemba losatha, ziwadzere kwa ana a Israele; popeza ndiyo nsembe yokweza; ndipo ikhale nsembe yokweza yodzera kwa ana a Israele, ya kwa nsembe zamtendere zao, ndiyo nsembe yao yokweza ya Yehova.
Ndipo Aroni anadzitengera Eliseba, mwana wamkazi wa Aminadabu, mlongo wake wa Nasoni, akhale mkazi wake; ndipo anambalira Nadabu ndi Abihu, Eleazara ndi Itamara.
Ndipo ana a Israele, ndilo khamu lonse, analowa m'chipululu cha Zini mwezi woyamba; ndipo anthu anakhala mu Kadesi; kumeneko anafa Miriyamu, naikidwa komweko.
nuvule Aroni zovala zake, numveke Eleazara mwana wake; ndipo Aroni adzaitanidwa kunka kwa anthu a mtundu wake, nadzafa komweko.
Pamenepo Mose anachita monga adamulamula Yehova; ndipo anakwera m'phiri la Hori pamaso pa khamu lonse.
Utaliona iwenso udzaitanidwa kunka kwa anthu a mtundu wako, monga anaitanidwa Aroni mbale wako;
Ndipo ana a Israele anayenda ulendo wao kuchokera ku zitsime za ana a Yaakani kufikira ku Mosera. Kumeneko anamwalira Aroni, ndi kumeneko anamuika; ndipo Eleazara mwana wake anachita ntchito ya nsembe m'malo mwake.
Ndipo Yoswa mwana wa Nuni anadzala ndi mzimu wanzeru; popeza Mose adamuikira manja ake; ndi ana a Israele anamvera iye, nachita monga Yehova adauza Mose.
Eleazaranso mwana wa Aroni anafa; ndipo anamuika paphiri la Finehasi mwana wake, limene adampatsa ku mapiri a Efuremu.