nuvule Aroni zovala zake, numveke Eleazara mwana wake; ndipo Aroni adzaitanidwa kunka kwa anthu a mtundu wake, nadzafa komweko.
Numeri 20:27 - Buku Lopatulika Pamenepo Mose anachita monga adamulamula Yehova; ndipo anakwera m'phiri la Hori pamaso pa khamu lonse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo Mose anachita monga adamulamula Yehova; ndipo anakwera m'phiri la Hori pamaso pa khamu lonse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mose adachitadi zimene Chauta adamlamula. Atatu onsewo adakwera phiri la Horo, mpingo wonse ukupenya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mose anachita monga Yehova anamulamulira: Anapita ku phiri la Hori gulu lonse likuona. |
nuvule Aroni zovala zake, numveke Eleazara mwana wake; ndipo Aroni adzaitanidwa kunka kwa anthu a mtundu wake, nadzafa komweko.
Ndipo Mose anavula Aroni zovala zake, naveka Eleazara mwana wake; ndipo Aroni anafa pomwepo pamwamba paphiri. Pamenepo Mose ndi Eleazara anatsika m'phirimo.
Ndipo anayenda ulendo kuchokera kuphiri la Hori, nadzera njira ya Nyanja Yofiira, kupaza ku dziko la Edomu; ndi mtima wa anthu unada chifukwa cha njirayo.