mwana wa Abisuwa mwana wa Finehasi, mwana wa Eleazara, mwana wa Aroni wansembe wamkulu.
Numeri 20:25 - Buku Lopatulika Tenga Aroni ndi Eleazara mwana wake, nukwere nao m'phiri la Hori; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tenga Aroni ndi Eleazara mwana wake, nukwere nao m'phiri la Hori; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Utenge Aroni pamodzi ndi Eleazara mwana wake, ukwere nawo pamwamba pa phiri la Horo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tenga Aaroni ndi mwana wake wamwamuna Eliezara ndipo ukwere nawo ku phiri la Hori. |
mwana wa Abisuwa mwana wa Finehasi, mwana wa Eleazara, mwana wa Aroni wansembe wamkulu.
Ndipo Mose anati kwa Aroni, ndi kwa Eleazara ndi Itamara ana ake, Musawinda tsitsi, musang'amba zovala zanu; kuti mungafe, ndi kuti angakwiye Iye ndi khamu lonse; koma abale anu, mbumba yonse ya Israele, alire chifukwa cha motowu Yehova anauyatsa.
Koma Nadabu ndi Abihu anafa pamaso pa Yehova muja anabwera nao moto wachilendo pamaso pa Yehova, m'chipululu cha Sinai, ndipo analibe ana; koma Eleazara ndi Itamara anachita ntchito ya nsembe pamaso pa atate wao Aroni.
Ndipo ana a Israele anayenda ulendo wao kuchokera ku zitsime za ana a Yaakani kufikira ku Mosera. Kumeneko anamwalira Aroni, ndi kumeneko anamuika; ndipo Eleazara mwana wake anachita ntchito ya nsembe m'malo mwake.