Ndi mbali ya kumwera kuloza kumwera ndiyo kuyambira ku Tamara kufikira ku madzi a Meribati-Kadesi, ku mtsinje wa Ejipito, ndi ku Nyanja Yaikulu. Ndiyo mbali ya kumwera kuloza kumwera.
Numeri 20:22 - Buku Lopatulika Ndipo anayenda ulendo kuchokera ku Kadesi; ndi ana a Israele, ndilo khamu lonse, anadza kuphiri la Hori. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anayenda ulendo kuchokera ku Kadesi; ndi ana a Israele, ndilo khamu lonse, anadza kuphiri la Hori. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono mpingo wonse wa Aisraele udanyamuka ku Kadesi kuja nukafika ku phiri la Horo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Gulu lonse la Aisraeli linachoka ku Kadesi ndipo linafika ku phiri la Hori. |
Ndi mbali ya kumwera kuloza kumwera ndiyo kuyambira ku Tamara kufikira ku madzi a Meribati-Kadesi, ku mtsinje wa Ejipito, ndi ku Nyanja Yaikulu. Ndiyo mbali ya kumwera kuloza kumwera.
Ndi ku malire a Gadi, mbali ya kumwera, kuloza kumwera, malire akhale kuyambira ku Tamara kufikira ku madzi a Meribati-Kadesi, ku mtsinje wa Ejipito, kufikira ku Nyanja Yaikulu.
Ndipo anamuka, nadza kwa Mose, ndi Aroni, ndi khamu lonse la ana a Israele, ku chipululu cha Parani ku Kadesi; ndipo anabwezera mau iwowa, ndi khamu lonse, nawaonetsa zipatso za dzikoli.
Ndipo ana a Israele, ndilo khamu lonse, analowa m'chipululu cha Zini mwezi woyamba; ndipo anthu anakhala mu Kadesi; kumeneko anafa Miriyamu, naikidwa komweko.
Pamenepo Mose anatumiza amithenga ochokera ku Kadesi kumuka kwa mfumu ya Edomu, ndi kuti, Atero mbale wanu Israele, Mudziwa zowawa zonse zinatigwera;
Pamenepo tinafuulira kwa Yehova, ndipo anamva mau athu, natuma mthenga, natitulutsa mu Ejipito; ndipo, taonani, tili mu Kadesi, ndiwo mzinda wa malekezero a malire anu.
Ndipo anayenda ulendo kuchokera kuphiri la Hori, nadzera njira ya Nyanja Yofiira, kupaza ku dziko la Edomu; ndi mtima wa anthu unada chifukwa cha njirayo.