Ndipo anthu ambiri osokonezeka anakwera nao; ndi nkhosa ndi ng'ombe, zoweta zambirimbiri.
Numeri 20:19 - Buku Lopatulika Ndipo ana a Israele ananena naye, Tidzatsata mseu; ndipo tikakamwa madzi ako, ine ndi zoweta zanga, pamenepo ndidzapatsa mtengo wake; sindifuna kanthu kena koma kungopitapo mwa njira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ana a Israele ananena naye, Tidzatsata mseu; ndipo tikakamwa madzi ako, ine ndi zoweta zanga, pamenepo ndidzapatsa mtengo wake; sindifuna kanthu kena koma kungopitapo mwa njira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Aisraele adamuuza kuti, “Ife tidzangodzera mu mseu waukulu mokhamo. Ngati ife ndi zoŵeta zathu timwako madzi anu, tidzalipira. Mungotilola kuti tidutse chabe.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Aisraeli anayankha kuti, “Tidzayenda motsata msewu waukulu. Ndipo ngati ife kapena ziweto zathu tidzamwa madzi anu tidzalipira. Tikungofuna tidutse nawo, palibenso china.” |
Ndipo anthu ambiri osokonezeka anakwera nao; ndi nkhosa ndi ng'ombe, zoweta zambirimbiri.
Undigulitse chakudya ndi ndalama, kuti ndidye; ndi kundipatsa madzi kwa ndalama, kuti ndimwe; chokhachi ndipitire choyenda pansi;
Ndipo ng'ombezo zinatsata njira yolunjika ku Betesemesi, zinali kuyenda mumseu, zilikulira; sizinapatukire ku dzanja lamanja, kapena kulamanzere; ndipo mafumu a Afilisti anazitsatira kufikira ku malire a Betesemesi.