Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Numeri 19:15 - Buku Lopatulika

Ndi zotengera zonse zovundukuka, zopanda chivundikiro chomangikapo, zili zodetsedwa.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndi zotengera zonse zovundukuka, zopanda chivundikiro chomangikapo, zili zodetsedwa.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Ndipo chiŵiya chilichonse chopanda chivundikiro nchoipitsidwa.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

ndiponso chiwiya chilichonse chopanda chivundikiro chidzakhala chodetsedwa.

Onani mutuwo



Numeri 19:15
6 Mawu Ofanana  

Ndipo chilichonse chakufa cha izi chikagwera kanthu, kanthuka kadzakhala kodetsedwa; ngakhale chipangizo chamtengo, kapena chovala, kapena chikopa kapena thumba, chipangizo chilichonse chimene agwira nacho ntchito, achiviike m'madzi, ndipo chidzakhala chodetsedwa kufikira madzulo; pamenepo chidzakhala choyera.


Ndipo chilichonse cha izi chikagwa m'chotengera chilichonse chadothi, chinthu chokhala m'mwemo chidetsedwa, ndi chotengeracho muchiswe.


Ndipo wansembe aziuza kuti atulutse zonse za m'nyumba, asanalowe kudzaona nthendayi, zinthu zonse zili m'nyumba zingakhale zodetsedwa; ndipo atatero wansembe alowe kukaona nyumbayi;


Chilamulo ndi ichi: Munthu akafa m'hema, yense wakulowa m'hemamo, ndi yense wakukhala m'hemamo, adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri.


Ndipo aliyense wakukhudza munthu wophedwa ndi lupanga, kapena mtembo, kapena fupa la munthu, kapena manda, pathengo poyera, adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri.


Muyeretse zovala zanu zonse, zipangizo zonse zachikopa, ndi zoomba zonse za ubweya wa mbuzi, ndi zipangizo zonse za mtengo.