Ndi a nyumba ya Israele adzapititsa miyezi isanu ndi iwiri alikuwaika, kuti ayeretse dziko.
Numeri 19:14 - Buku Lopatulika Chilamulo ndi ichi: Munthu akafa m'hema, yense wakulowa m'hemamo, ndi yense wakukhala m'hemamo, adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chilamulo ndi ichi: Munthu akafa m'hema, yense wakulowa m'hemamo, ndi yense wakukhala m'hemamo, adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Pamene munthu afera m'hema, lamulo lake nali: munthu aliyense amene aloŵa m'hemamo, ndipo aliyense amene ali m'hema, akhale woipitsidwa masiku asanu ndi aŵiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Pamene munthu wamwalira mu tenti, lamulo lomwe ligwire ntchito ndi ili: Aliyense wolowa mu tentimo ndi amene anali momwemo adzakhala odetsedwa kwa masiku asanu ndi awiri, |
Ndi a nyumba ya Israele adzapititsa miyezi isanu ndi iwiri alikuwaika, kuti ayeretse dziko.
Ichi ndi chilamulo cha wakukha, ndi cha iye wakugona uipa, kuti kumkhalitse wodetsedwa;
Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Nena ndi ansembe, ana a Aroniwo, nuti nao, Asadzidetse mmodzi wa inu chifukwa cha wakufa mwa anthu a mtundu wake;
Aliyense wakukhudza mtembo wa munthu aliyense wakufa, osadziyeretsa, aipsa chihema cha Yehova; amsadze munthuyo kwa Israele; popeza sanamwaze madzi akusiyanitsa; ndiye wodetsedwa; kudetsedwa kwake kukali pa iye.
Muyeretse zovala zanu zonse, zipangizo zonse zachikopa, ndi zoomba zonse za ubweya wa mbuzi, ndi zipangizo zonse za mtengo.
Uza ana a Israele kuti azitulutsa m'chigono akhate onse, ndi onse akukhala nako kukha, ndi onse odetsedwa chifukwa cha akufa;
Munthu akafa chikomo pali iye, ndipo akadetsa mutu wake wowinda; pamenepo azimeta mutu wake tsiku la kumyeretsa kwake, tsiku lachisanu ndi chiwiri aumete.
Pamenepo panali amuna, anadetsedwa ndi mtembo wa munthu, ndipo sanakhoze kuchita Paska tsiku lomwelo; m'mwemo anafika pamaso pa Mose ndi pamaso pa Aroni tsiku lomwelo;