Chifukwa chake unene nao, Pamene mukwezako zokometsetsa zake, zidzayesedwanso kwa Alevi ngati zipatso za padwale, ndi zipatso za mopondera mphesa.
Numeri 18:31 - Buku Lopatulika Ndipo muzidye pamalo ponse, inu ndi a pabanja panu; popeza ndizo mphotho yanu mwa ntchito yanu m'chihema chokomanako. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo muzidye pamalo ponse, inu ndi a pabanja panu; popeza ndizo mphotho yanu mwa ntchito yanu m'chihema chokomanako. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mungathe kuzidyera pa malo aliwonse, inuyo ndi a m'banja mwanu. Zimenezo ndi mphotho yanu chifukwa cha ntchito imene mumagwira m'chihema chamsonkhano. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inu ndi a pa banja panu mungathe kudyera zimenezi paliponse chifukwa ndi malipiro a ntchito yanu ya ku tenti ya msonkhano. |
Chifukwa chake unene nao, Pamene mukwezako zokometsetsa zake, zidzayesedwanso kwa Alevi ngati zipatso za padwale, ndi zipatso za mopondera mphesa.
Ndipo simudzasenzapo uchimo, mutakwezako zokometsetsa zake; ndipo musamaipsa zinthu zopatulika za ana a Israele, kuti mungafe.
kapena thumba la kamba la kunjira, kapena malaya awiri, kapena nsapato, kapena ndodo; pakuti wantchito ayenera kulandira zakudya zake.
Ndipo m'nyumba momwemo khalani, ndi kudya ndi kumwa za kwao; pakuti wantchito ayenera mphotho yake; musachokachoka m'nyumba.
Pakuti kuli chiyani chimene munachepetsedwa nacho ndi Mipingo yotsala ina, ngati si ichi kuti ine ndekha sindinasaukitse inu? Ndikhululukireni choipa ichi.