katengeni atate wanu ndi mabanja anu, nimudze kwa ine; ndipo ndidzakupatsani inu zabwino za dziko la Ejipito, ndipo mudzadya zonenepa za dzikoli.
Numeri 18:29 - Buku Lopatulika Mupereke nsembe zokweza zonse za Yehova kuzitenga ku mphatso zanu zonse, kusankhako zokometsetsa ndizo zopatulika zake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mupereke nsembe zokweza zonse za Yehova kuzitenga ku mphatso zanu zonse, kusankhako zokometsetsa ndizo zopatulika zake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pa mphatso zonse zimene mwalandira, mupatuleko zake za Chauta, ndipo zimene mwapatulazo zikhale zabwino kopambana zina zonse.’ Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Muyenera kupereka monga gawo la Yehova magawo abwino kwambiri ndi opatulika a chilichonse chimene chapatsidwa kwa inu.’ |
katengeni atate wanu ndi mabanja anu, nimudze kwa ine; ndipo ndidzakupatsani inu zabwino za dziko la Ejipito, ndipo mudzadya zonenepa za dzikoli.
ndipo zikhale za Aroni ndi za ana ake aamuna, mwa lemba losatha, ziwadzere kwa ana a Israele; popeza ndiyo nsembe yokweza; ndipo ikhale nsembe yokweza yodzera kwa ana a Israele, ya kwa nsembe zamtendere zao, ndiyo nsembe yao yokweza ya Yehova.
Momwemo inunso muzipereka kwa Yehova nsembe yokweza yochokera ku magawo anu onse a magawo khumi, a zonse muzilandira kwa ana a Israele; ndipo muperekeko nsembe yokweza ya Yehova kwa Aroni wansembe.
Chifukwa chake unene nao, Pamene mukwezako zokometsetsa zake, zidzayesedwanso kwa Alevi ngati zipatso za padwale, ndi zipatso za mopondera mphesa.