Ndipo Melkizedeki mfumu ya ku Salemu, anatuluka nao mkate ndi vinyo: iye ndiye wansembe wa Mulungu Wamkulukulu.
Numeri 18:28 - Buku Lopatulika Momwemo inunso muzipereka kwa Yehova nsembe yokweza yochokera ku magawo anu onse a magawo khumi, a zonse muzilandira kwa ana a Israele; ndipo muperekeko nsembe yokweza ya Yehova kwa Aroni wansembe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Momwemo inunso muzipereka kwa Yehova nsembe yokweza yochokera ku magawo anu onse a magawo khumi, a zonse muzilandira kwa ana a Israele; ndipo muperekeko nsembe yokweza ya Yehova kwa Aroni wansembe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho inunso muzipereka zopereka zanu kwa Chauta, zotapa pa chachikhumi chilichonse chimene mulandira kwa Aisraele. Pa zimene mwalandirazo mutengeko mphatso ya Chauta, ndipo mupatse wansembe Aroni. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwa njira imeneyi inunso muzipereka chopereka kwa Yehova kuchokera ku chakhumi chanu chilichonse chimene mumalandira kuchokera kwa Aisraeli. Kuchokera ku chakhumicho muziperekako gawo la Yehova kwa Aaroni, wansembe. |
Ndipo Melkizedeki mfumu ya ku Salemu, anatuluka nao mkate ndi vinyo: iye ndiye wansembe wa Mulungu Wamkulukulu.
Ndipo akuyesereninso nsembe yanu yokweza monga tirigu wa padwale, monga mopondera mphesa modzala.
Mupereke nsembe zokweza zonse za Yehova kuzitenga ku mphatso zanu zonse, kusankhako zokometsetsa ndizo zopatulika zake.
Uzitenge ku gawo lao, ndi kuzipereka kwa Eleazara wansembe, zikhale nsembe yokweza ya Yehova.
m'mene Yesu mtsogoleri analowamo chifukwa cha ife, atakhala mkulu wa ansembe nthawi yosatha monga mwa dongosolo la Melkizedeki.