Azidya nsembe yaufa, ndi nsembe yauchimo, ndi nsembe yopalamula; ndipo zilizonse zoperekedwa chiperekere mu Israele ndi zao.
Numeri 18:14 - Buku Lopatulika Zilizonse zoperekedwa chiperekere mu Israele ndi zako. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Zilizonse zoperekedwa chiperekere m'Israele ndi zako. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chinthu chilichonse chimene anthu amapatulira Chauta m'dziko la Israele chikhale chanu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Chilichonse mu Israeli chomwe chapatulidwira Yehova ndi chako. |
Azidya nsembe yaufa, ndi nsembe yauchimo, ndi nsembe yopalamula; ndipo zilizonse zoperekedwa chiperekere mu Israele ndi zao.
koma potuluka m'chaka choliza lipenga, mundawo ukhale wopatulikira Yehova, ngati munda woperekedwa chiperekere kwa Mulungu; ukhale wakewake wa wansembe.
Koma asachigulitse kapena kuchiombola chinthu choperekedwa chiperekere kwa Mulungu, chimene munthu achipereka chiperekere kwa Yehova, chotengako ku zonse ali nazo, ngakhale munthu, kapena nyama, kapena munda wakewake; chilichonse choperekedwa chiperekere kwa Mulungu nchopatulika kwambiri.