Ndipo kunakhala, pakunena Aroni ndi khamu lonse la ana a Israele kuti iwo anatembenukira kuchipululu, ndipo, taonani, ulemerero wa Yehova unaoneka mumtambo.
Numeri 16:42 - Buku Lopatulika Ndipo kunali, posonkhanidwa khamulo kutsutsana nao Mose ndi Aroni, kuti anacheukira chihema chokomanako; taonani, mtambo unachiphimba, ndi ulemerero wa Yehova unaoneka. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo kunali, posonkhanidwa khamulo kutsutsana nao Mose ndi Aroni, kuti anacheukira chihema chokomanako; taonani, mtambo unachiphimba, ndi ulemerero wa Yehova unaoneka. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene mpingo udasonkhana kuti uukire Mose ndi Aroni, anthuwo adatembenuka ndi kuyang'ana ku chihema chamsonkhano. Tsono adangoona mtambo utaphimba chihemacho, ndipo ulemerero wa Chauta udaonekera. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma pamene anthuwo anasonkhana kuti atsutsane ndi Mose ndi Aaroni, atatembenuka kuyangʼana ku tenti ya msonkhano, mwadzidzidzi mtambo unaphimba tentiyo ndipo ulemerero wa Yehova unaonekera. |
Ndipo kunakhala, pakunena Aroni ndi khamu lonse la ana a Israele kuti iwo anatembenukira kuchipululu, ndipo, taonani, ulemerero wa Yehova unaoneka mumtambo.
ndi m'mawa mwake mudzaona ulemerero wa Yehova, popeza alinkumva mulikudandaulira Yehova; pakuti ife ndife chiyani, kuti mutidandaulira ife?
Ndipo ulemerero wa Yehova unakhalabe paphiri la Sinai, ndi mtambo unaliphimba masiku asanu ndi limodzi; ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri Iye ali m'kati mwa mtambo anaitana Mose.
Ndipo Mose ndi Aroni analowa ku chihema chokomanako, natuluka, nadalitsa anthu; ndipo ulemerero wa Yehova unaonekera kwa anthu onse.
Koma khamu lonse lidati liwaponye miyala. Ndipo ulemerero wa Yehova unaoneka m'chihema chokomanako kwa ana onse a Israele.
Ndipo Kora anasonkhanitsa khamu lonse mopikisana nao ku khomo la chihema chokomanako; ndipo ulemerero wa Yehova unaoneka kwa khamu lonse.
Ndipo Mose ndi Aroni anachoka pamaso pa msonkhano kunka ku khomo la chihema chokomanako, nagwa nkhope zao pansi; ndipo ulemerero wa Yehova unaonekera iwo.