Tsopano ndiwe wotembereredwa kunthaka, imene inatsegula pakamwa pake kulandira padzanja lako mwazi wa mphwako:
Numeri 16:32 - Buku Lopatulika ndi dziko linayasama pakamwa pake ndi kuwameza, iwo ndi mabanja ao, ndi amuna ao onse akutsata Kora, ndi akatundu ao onse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndi dziko linayasama pakamwa pake ndi kuwameza, iwo ndi mabanja ao, ndi amuna ao onse akutsata Kora, ndi akatundu ao onse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nthakayo idayasama ndi kuŵameza onsewo pamodzi ndi mabanja ao ndiponso anthu onse a gulu la Kora ndi zinthu zao zonse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ndipo dziko linatsekula pakamwa pake ndi kuwameza pamodzi ndi nyumba zawo ndi anthu onse a Kora ndi katundu wawo yense. |
Tsopano ndiwe wotembereredwa kunthaka, imene inatsegula pakamwa pake kulandira padzanja lako mwazi wa mphwako:
Dziko lapansi lasweka ndithu, dziko lapansi lasungunukadi, dziko lapansi lili kugwedezeka kopambana.
Ndipo manda akuza chilakolako chake, natsegula kukamwa kwake kosayeseka; ndi ulemerero wao, ndi unyinji wao, ndi phokoso lao, ndi iye amene akondwerera mwa iwo atsikira mommo.
nimutenge munthu yense mbale yake yofukizamo, nimuike chofukiza m'mwemo, nimubwere nazo, yense mbale yake yofukizamo pamaso pa Yehova, mbale zofukizamo mazana awiri ndi makumi asanu; ndi iwe, ndi Aroni, yense mbale yake yofukizamo.
Koma Yehova akalenga chinthu chatsopano, ndi nthaka ikayasama pakamwa pake, nikawameza ndi zonse ali nazo, nakatsikira iwo kumanda ali ndi moyo; pamenepo mudzadziwa kuti anthu awa anyoza Mulungu.
Chomwecho iwowa, ndi onse anali nao, anatsikira kumanda ali ndi moyo, ndi dziko linasunama pa iwo, ndipo anaonongeka pakati pa msonkhano.
Koma akufa nao mliri ndiwo zikwi khumi ndi zinai mphambu mazana asanu ndi awiri, osawerenga aja adafera chija cha Kora.
ndipo dziko linayasama pakamwa pake, ndi kuwameza pamodzi ndi Kora, pakufa msonkhano uja; muja moto unaononga amuna mazana awiri ndi makumi asanu, nakhala iwo chizindikiro.
Atate wathu adamwalira m'chipululu, ndipo sanakhale iye pakati pa msonkhano wa iwo akusonkhana kutsutsana ndi Yehova, mu msonkhano wa Kora; koma anafera zoipa zakezake; ndipo analibe ana aamuna.
ndi chimene anachitira Datani ndi Abiramu, ana a Eliyabu, mwana wa Rubeni; muja nthaka inatsegula pakamwa pake, ndi kuwameza iwo, ndi mabanja ao, ndi mahema ao, ndi za moyo zonse zakuwatsata pakati pa Israele wonse.
Ndipo dziko linathandiza mkaziyo, ndi dziko linatsegula m'kamwa mwake, nilinameza madzi a mtsinje amene chinjoka chinalavula m'kamwa mwake.