Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati,
Ndipo Chauta adauza Mose ndi Aroni kuti,
Yehova anawuza Mose ndi Aaroni kuti,
Koma nyumba ya Israele inapandukira Ine m'chipululu, sanayende m'malemba anga, nanyoza maweruzo anga, amene munthu akawachita adzakhala nao ndi moyo; ndi masabata anga anawaipsa kwambiri; pamenepo ndidati ndiwatsanulire ukali wanga m'chipululu kuwatha.
Ndipo Kora anasonkhanitsa khamu lonse mopikisana nao ku khomo la chihema chokomanako; ndipo ulemerero wa Yehova unaoneka kwa khamu lonse.
Dzipatuleni pakati pa khamu lino, kuti ndiwathe m'kamphindi.