Ndipo uzipanga zotayira zake zakulandira mapulusa ake, ndi zoolera zake, ndi mbale zowazira zake, ndi mitungo yake, ndi zopalira moto zake; zipangizo zake zonse uzipanga zamkuwa.
Numeri 16:17 - Buku Lopatulika nimutenge munthu yense mbale yake yofukizamo, nimuike chofukiza m'mwemo, nimubwere nazo, yense mbale yake yofukizamo pamaso pa Yehova, mbale zofukizamo mazana awiri ndi makumi asanu; ndi iwe, ndi Aroni, yense mbale yake yofukizamo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 nimutenge munthu yense mbale yake yofukizamo, nimuike chofukiza m'mwemo, nimubwere nazo, yense mbale yake yofukizamo pamaso pa Yehova, mbale zofukizamo mazana awiri ndi makumi asanu; ndi iwe, ndi Aroni, yense mbale yake yofukizamo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Aliyense mwa inu atenge chofukizira lubani, athiremo lubani. Nonsenu mubwere ku chihemacho, aliyense ndi chofukizira chake. Zofukizirazo zikhale 250, ndipo iweyo ndi Aroni mutenge aliyense chakechake.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Munthu aliyense akatenge chofukizira ndi kuyikamo lubani, zofukizira 250 zonse pamodzi ndi kuzibweretsa pamaso pa Yehova. Iwe ndi Aaroni mudzabweretsenso zofukizira zanu.” |
Ndipo uzipanga zotayira zake zakulandira mapulusa ake, ndi zoolera zake, ndi mbale zowazira zake, ndi mitungo yake, ndi zopalira moto zake; zipangizo zake zonse uzipanga zamkuwa.
Ndipo pamaso pao panaima amuna makumi asanu ndi awiri a akulu a nyumba ya Israele, ndi pakati pao panaima Yazaniya mwana wa Safani, munthu aliyense ndi mbale yake ya zofukiza m'dzanja lake; ndi fungo lake la mtambo wa zonunkhira linakwera.
Ndipo Mose anati kwa Kora, Iwe ndi khamu lako lonse mukhale pamaso pa Yehova mawa, iwe ndi iwowa, ndi Aroni;
Potero munthu yense anatenga mbale yake yofukizamo, naikamo moto, naikapo chofukiza, naima pa khomo la chihema chokomanako pamodzi ndi Mose ndi Aroni.
Chifukwa chake tsono, imani pano, kuti ndiweruzane nanu pamaso pa Yehova, za ntchito zonse zolungama za Yehova anakuchitirani inu ndi makolo anu.