Numeri 15:38 - Buku Lopatulika Nena ndi ana a Israele, nuwauze kuti adziombere mphonje m'mphepete mwa zovala zao, mwa mibadwo yao, naike pamphonje m'mphepetemo thonje lamadzi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Nena ndi ana a Israele, nuwauze kuti adziombere mphonje m'mphepete mwa zovala zao, mwa mibadwo yao, naike pamphonje m'mphepetemo thonje lamadzi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Lankhula ndi Aisraele, ndipo uŵauze kuti pa mibadwo yao yonse azisokerera mphonje pa ngodya za zovala, ndipo pa mphonje ya ngodya iliyonse asokerepo chingwe chobiriŵira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Yankhula ndi Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Pa mibado yanu yonse muzisokerera mphonje pa ngodya za zovala zanu ndipo pa ngodya ya mphonje iliyonse azisokererapo chingwe chobiriwira. |
Koma amachita ntchito zao zonse kuti aonekere kwa anthu; pakuti akulitsa chitando chake cha njirisi zao, nakulitsa mphonje,
Ndipo onani, mkazi, anali ndi nthenda yachidwalire zaka khumi ndi ziwiri, anadza pambuyo pake, nakhudza mphonje ya chofunda chake;
anadza pambuyo pake, nakhudza mphonje ya chovala chake; ndipo pomwepo nthenda yake inaleka.