natsitsitize mafuta otsala m'dzanja lake la wansembe, pamutu pa iye wakuti ayeretsedwe; ndipo wansembe amchitire chomtetezera pamaso pa Yehova.
Numeri 15:28 - Buku Lopatulika Ndipo wansembe achite chomtetezera munthu wakulakwa, osalakwa dala pamaso pa Yehova, kumchita chomtetezera; ndipo adzakhululukidwa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo wansembe achite chomtetezera munthu wakulakwa, osalakwa dala pamaso pa Yehova, kumchita chomtetezera; ndipo adzakhululukidwa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Motero wansembe amchitire mwambo wopepesera machimo pamaso pa Chauta munthu wolakwa mosadziŵayo. Akalakwa choncho mosadziŵa, amchitire mwambo wopepesera machimo, ndipo adzakhululukidwa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Wansembe apereke nsembe yopepesera machimowo pamaso pa Yehova chifukwa cha munthu yemwe anachimwa mosadziwayo. Nsembe yopepesera tchimo lakelo ikaperekedwa, munthuyo adzakhululukidwa. |
natsitsitize mafuta otsala m'dzanja lake la wansembe, pamutu pa iye wakuti ayeretsedwe; ndipo wansembe amchitire chomtetezera pamaso pa Yehova.
Lankhula ndi ana a Israele, ndi kuti, Munthu akachimwa, osati dala, pa china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova, nakachitapo kanthu;
Atero nayo ng'ombeyo; monga umo anachitira ng'ombe ya nsembe yauchimo; ndipo wansembe awachitire chowatetezera, ndipo adzakhululukidwa.
nawachotse mafuta ake onse, monga umo amachotsera mafuta a nkhosa pa nsembe yoyamika; ndipo wansembeyo atenthe awa paguwa la nsembe, monga umo amachitira nsembe zamoto za Yehova; ndipo wansembeyo amchitire chomtetezera pa kuchimwa kwake adakuchimwira, ndipo adzakhululukidwa.
Kunena za wobadwa m'dziko mwa ana a Israele, ndi mlendo wakukhala pakati pao, mukhale nacho chilamulo chimodzi kwa iye wakuchita kanthu kosati dala.