Lankhula ndi ana a Israele, ndi kuti, Munthu akachimwa, osati dala, pa china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova, nakachitapo kanthu;
Numeri 15:26 - Buku Lopatulika Ndipo khamu lonse la ana a Israele, adzakhululukidwa, ndi mlendo yemwe wakukhala pakati pao; popeza khamu lonse linachichita osati dala. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo khamu lonse la ana a Israele, adzakhululukidwa, ndi mlendo yemwe wakukhala pakati pao; popeza khamu lonse linachichita osati dala. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa mpingo wonse wa Aisraele udzakhululukidwa pamodzi ndi mlendo yemwe amene akhala pakati pao, poti anthu onse adalakwa mosadziŵa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Gulu lonse la Aisraeli ndi alendo okhala pakati pawo adzakhululukidwa chifukwa anthu onsewo anachimwa mosadziwa. |
Lankhula ndi ana a Israele, ndi kuti, Munthu akachimwa, osati dala, pa china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova, nakachitapo kanthu;
pamenepo kudzali, ngati anachichita osati dala, osachidziwa khamulo, khamu lonse lipereke ng'ombe yamphongo ikhale nsembe yopsereza, ya fungo lokoma ya Yehova, pamodzi ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe yake yothira, monga mwa chiweruzo chake; ndi tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo.