popeza adzamva za dzina lanu lalikulu ndi dzanja lanu lamphamvu ndi mkono wanu wotambasuka; akabwera iyeyo nadzapemphera molunjika kunyumba ino;
Numeri 15:14 - Buku Lopatulika Ndipo akakhala nanu mlendo, kapena aliyense wakukhala pakati pa inu mwa mibadwo yanu, nakachitira Yehova nsembe yamoto ya fungo lokoma; monga muchita inu, momwemo iyenso, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo akakhala nanu mlendo, kapena aliyense wakukhala pakati pa inu mwa mibadwo yanu, nakachitira Yehova nsembe yamoto ya fungo lokoma; monga muchita inu, momwemo iyenso, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ngati ndi mlendo amene akhala pakati panu, kapena wina aliyense amene akhala pakati panu pa mibadwo yanu yonse, ndipo afuna kupereka nsembe yotentha pa moto, yotulutsa fungo lokomera Chauta, azichita monga momwe muchitira inu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ku mibado yanu yonse ya mʼtsogolo, pamene mlendo kapena wina aliyense wokhala pakati panu apereka chopereka chotentha pa moto kuti chikhale fungo lokoma kwa Yehova, azichita mofanana ndi momwe inu mumachitira. |
popeza adzamva za dzina lanu lalikulu ndi dzanja lanu lamphamvu ndi mkono wanu wotambasuka; akabwera iyeyo nadzapemphera molunjika kunyumba ino;
Nena ndi Aroni, ndi ana ake aamuna, ndi ana onse a Israele, nuti nao, Aliyense wa mbumba ya Israele, kapena wa alendo ali mu Israele, akabwera nacho chopereka chake, monga mwa zowinda zao zonse, kapena monga mwa zopereka zaufulu zao, zimene abwera nazo kwa Yehova zikhale nsembe zopsereza;
Ndipo musamazilandira izi ku dzanja la mlendo ndi kubwera nazo zikhale chakudya cha Mulungu wanu; popeza zili nako kuvunda kwao; zili ndi chilema; sizidzalandirikira inu.
Onse akubadwa m'dzikomo achite izi momwemo, pobwera nayo kwa Yehova nsembe yamoto ya fungo lokoma.
Kunena za khamu, pakhale lemba limodzi kwa inu, ndi kwa mlendo wakukhala kwanu, ndilo lemba losatha mwa mibadwo yanu; monga mukhala inu, momwemo mlendo pamaso pa Yehova.