Ndipo pamene anthu anamva mau awa oipa anachita chisoni; ndipo panalibe mmodzi anavala zokometsera zake.
Numeri 14:39 - Buku Lopatulika Ndipo Mose anauza ana a Israele mau onse awa; ndipo anthu anamva chisoni chambiri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mose anauza ana a Israele mau onse awa; ndipo anthu anamva chisoni chambiri. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mose adaŵafotokozera Aisraele mau onseŵa, ndipo anthu adalira kwambiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mose atafotokoza izi kwa Aisraeli onse, anthuwo analira kwambiri. |
Ndipo pamene anthu anamva mau awa oipa anachita chisoni; ndipo panalibe mmodzi anavala zokometsera zake.
Nunene nao, Pali Ine ati Yehova, ndidzachitira inu ndithu monga mwanena m'makutu mwanga;
Koma Yoswa mwana wa Nuni, ndi Kalebe mwana wa Yefune, anakhala ndi moyo mwa amuna aja adamukawo kukazonda dziko.
koma anawo a Ufumu adzatayidwa kumdima wakunja; komweko kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.
Pakuti mudziwa kutinso pamene anafuna kulowa dalitsolo, anakanidwa (pakuti sanapeze malo akulapa), angakhale analifunafuna ndi misozi.
Mwa ichi ana a Israele sangathe kuima pamaso pa adani ao, awafulatira adani ao, pakuti aperekedwa aonongeke. Sindidzakhalanso nanu mukapanda kuononga choperekedwacho, kuchichotsa pakati pa inu.